Jeremiah 24:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndikunena kuti, Akapolo a ku Yuda amene ndidaŵachotsa ku malo ano, kupita nawo ku dziko la Ababiloni, ndikuŵafanizira ndi nkhuyu zabwinozi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa Yehova, Mulungu wa Israele, atero, Monga nkhuyu zabwino izi, momwemo ndidzasamalira am'nsinga a Yuda, amene ndawachotsera m'malo muno kunka kudziko la Ababiloni, kuwachitira bwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, ‘Anthu a ku Yuda amene ndinawachotsa ku malo ano nʼkupita nawo ku ukapolo ku dziko la Ababuloni ndikuwafanizira ndi nkhuyu zabwinozi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa Yehova, Mulungu wa Israyeli, atero, Monga nkhuyu zabwino izi, momwemo ndidzasamalira am'nsinga a Yuda, amene ndawacotsera m'malo muno kunka ku dziko la Akasidi, kuwacitira bwino.