Jeremiah 24:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzachita chotheka kuti ndiŵachitire zabwino ndi kuŵabwezeranso ku dziko lao. Ndidzaŵamanga osati kuŵapasula. Ndidzaŵakhazikitsa, osati kuŵazula ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndidzaika maso anga pa iwo kuti ndiwachitire iwo bwino, ndipo ndidzawabwezanso kudziko ili: ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, osawapasula; ndi kuwabzala, osawazula iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzaonetsesa kuti ndiwachitire zabwino ndipo ndidzabwera nawonso ku dziko lino. Ndidzawamanga osati kuwapasula; ndidzawadzala osati kuwazula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndidzaika maso anga pa iwo kuti ndiwacitire iwo bwino, ndipo ndidzawabwezanso ku dziko ili: ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, osawapasula; ndi kuwabzyala, osawazula iwo.