Jeremiah 24:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma monga nkhuyu zoipa zija, zosatinso kudyekazi, ndimo m'mene ndidzalangire Zedekiya mfumu ya ku Yuda, pamodzi ndi akalonga, ndi onse otsala a mu Yerusalemu amene ali m'dziko lino, ndiponso Ayuda amene akukhala m'dziko la Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo monga nkhuyu zoipa, zosadyeka, poti nzoipa; ntheradi atero Yehova, Chomwecho ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi akulu ake, ndi otsala a m'Yerusalemu, amene atsala m'dziko ili, ndi amene akhala m'dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Koma monga nkhuyu zoyipa zija, zomwe ndi zoyipa kwambiri zosati nʼkudya,’ Yehova akuti, ‘ndi mmene ndidzalangire Zedekiya mfumu ya ku Yuda, nduna zake pamodzi ndi otsala a mu Yerusalemu, kaya adzakhala ali mʼdziko muno kapena mʼdziko la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo, monga nkhuyu zoipa, zosadyeka, poti nzoipa; ntheradi atero Yehova, Comweco ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi akulu ace, ndi otsala a m'Yerusalemu, amene atsala m'dziko ili, ndi amene akhala m'dziko la Aigupto.