Jeremiah 24:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaŵasandutsa chinthu chonyansa kwa anthu a maufumu onse a pa dziko lapansi, chinthu chonyozeka, chinthu chopanda pake, chinthu chomachiseka ndi chotembereredwa kulikonse kumene ndidzaŵapirikitsire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzawapatsa akhale choopsetsa choipa ku maufumu a dziko lapansi; akhale chitonzo ndi nkhani ndi choseketsa, ndi chitemberero, monse m'mene ndidzawapirikitsiramo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawasandutsa chinthu chonyansa kwa maufumu onse a dziko lapansi, chinthu chonyozeka ndi chopandapake, chinthu chochitidwa chipongwe ndi chotembereredwa kulikonse kumene ndidzawabalalitsira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzawapatsa akhale coopsetsa coipa ku maufumu a dziko lapansi; akhale citonzo ndi nkhani ndi coseketsa, ndi citemberero, monse m'mene ndidzawapitikitsiramo.