Jeremiah 25:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Naŵa mau amene adadza kwa Yeremiya, onena za anthu onse a ku Yuda. Mauŵa adafika chaka chachinai cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, ndiye kuti chaka choyamba cha ufumu wa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mau amene anadza kwa Yeremiya za anthu onse a Yuda chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda; ndicho chaka choyamba cha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anayankhula ndi Yeremiya za anthu onse a ku Yuda mʼchaka chachinayi cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, chimene chinali chaka choyamba cha ufumu wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mau amene anadza kwa Yeremiya za anthu onse a Yuda caka cacinai ca Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda; ndico caka coyamba ca Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo;