Jeremiah 25:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zaka makumi asanu ndi aŵirizo zitatha, ndidzailanga mfumu ya ku Babiloniyo pamodzi ndi anthu ake chifukwa cha zoipa zao, ndipo dziko lao ndidzalisandutsa bwinja mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzakhala, zitapita zaka makumi asanu ndi awiri, ndidzalanga mfumu ya ku Babiloni, ndi mtundu uja womwe, ati Yehova, chifukwa cha mphulupulu zao, ndi dziko la Ababiloni; ndipo ndidzaliyesa mabwinja amuyaya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma zaka 70 zikadzatha, ndidzalanga mfumu ya ku Babuloni pamodzi ndi anthu ake, chifukwa cha zolakwa zawo,” akutero Yehova, “ndipo dziko lawo lidzakhala chipululu mpaka muyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzakhala, zitapita zaka makumi asanu ndi awiri, ndzidzalanga mfumu ya ku Babulo, ndi mtundu uja womwe, ati Yehova, cifukwa ca mphulupulu zao, ndi dziko la Akasidi; ndipo ndidzaliyesa mabwinja amuyaya.