Jeremiah 25:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzachita zonse zimene ndidanena zokhudza dziko limenelo, zonse zimene zidalembedwa m'bukumu, ndiponso zonse zimene mneneri Yeremiya adalosa zotsutsa anthu ameneŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzatengera dzikolo mau anga onse amene ndinanenera ilo, mau onse olembedwa m'buku ili, amene Yeremiya wanenera mitundu yonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzachita zinthu zonse zimene ndinayankhula zotsutsa dzikolo, zonse zimene zalembedwa mʼbuku lino, ndiponso zonse zimene Yeremiya analosera zotsutsa anthu amenewa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzatengera dzikolo mau anga onse amene ndinanenera ilo, mau onse olembedwa m'buku ili, amene Yeremiya wanenera mitundu yonse.