Jeremiah 25:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, Mulungu wa Israele, adandiwuza kuti, “Tenga chikho ichi chodzaza ndi mkwiyo wanga, ndipo ukamwetse anthu a mitundu yonse kumene nditi ndikutume.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Yehova, Mulungu wa Israele, atero kwa ine, Tenga chikho cha vinyo wa ukaliwu pa dzanja langa, ndi kumwetsa mitundu yonse, imene ndikutumizirako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova, Mulungu wa Israeli, anandiwuza kuti, “Tenga chikho ichi chodzaza ndi vinyo wa ukali wanga, ndipo ukamwetse anthu a mitundu yonse kumene ndikukutuma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Yehova, Mulungu wa Israyeli, atero kwa ine, Tenga cikho ca vinyo wa ukaliwu pa dzanja langa, ndi kumwetsa mitundu yonse, imene ndikutumizirako.