Jeremiah 25:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adandituma ku Yerusalemu, ku mizinda ya ku Yuda, kwa mafumu ake ndi kwa akalonga ake, kuti ndiŵasandutse ngati bwinja, ndi chinthu chonyozeka ndi chomachiseka monga m'mene aliri tsopanomu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yerusalemu, ndi midzi ya Yuda, ndi mafumu ake omwe, ndi akulu ake, kuwayesa iwo bwinja, chizizwitso, chotsonyetsa, ndi chitemberero; monga lero lino;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anandituma ku Yerusalemu ndi ku mizinda ya Yuda, kwa mafumu ake ndi nduna zake kuti ndikawasandutse ngati bwinja ndi chinthu chochititsa mantha ndi chonyozeka ndiponso chotembereredwa, monga mmene alili lero lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yerusalemu, ndi midzi ya Yuda, ndi mafumu ace omwe, ndi akuru ace, kuwayesa iwo bwinja, cizizwitso, cotsonyetsa, ndi citemberero; monga lero lino;