Jeremiah 25:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kwa mafumu onse akumpoto, akufupi ndi akutali omwe, ndi kwa maufumu onse a dziko lonse lapansi. Potsiriza, atamwa onsewo, idzamwe ndi mfumu ya ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi mafumu onse a kumpoto, a kutali ndi a kufupi, wina ndi mnzake; ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala pansi pano; ndi mfumu ya Sesaki adzamwa pambuyo pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndiponso kwa mafumu onse a kumpoto, akufupi ndi kutali omwe, mafumu onse a dziko lapansi. Ndipo potsiriza pake, idzamwenso ndi mfumu Sesaki.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi mafumu onse a kumpoto, a kutari ndi a kufupi, wina ndi mnzace; ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala pansi pano; ndi mfumu ya Sesaki adzamwa pambuyo pao.