Jeremiah 25:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopanotu ndiyamba ndalanga mzinda umene umadziŵika ndi dzina langa. Kodi mukuganiza kuti inuyo simudzalangidwa? Iyai, simungathe kupulumuka. Ndithu, nditumiza nkhondo kwa anthu onse okhala pa dziko lapansi,” akutero Chauta Wamphamvuzonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti, taonani, ndiyamba kuchita choipa pa mudzi umene utchedwa ndi dzina langa, kodi inu mudzakhala osalangidwa konse? Simudzakhala osalangidwa; pakuti ndidzaitana lupanga ligwe pa onse okhala m'dziko lapansi, ati Yehova wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, tsopano ndiyamba kulanga mzinda uno umene umadziwika ndi dzina langa. Kodi inu muganiza kuti simudzalangidwa? Ayi, simudzapulumuka chifukwa ndikutumiza nkhondo pa onse okhala pa dziko lapansi, akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti, taonani, ndiyamba kucita coipa pa mudzi umene uchedwa ndi dzina langa, kodi inu mudzakhala osalangidwa konse? Simudzakhala osalangidwa; pakuti ndidzaitana lupanga ligwe pa onse okhala m'dziko lapansi, ati Yehova wa makamu.