Jeremiah 25:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono iwe, ulengeze mau oŵatsutsa, uŵauze kuti, ‘Chauta adzakhuluma kumwamba, mau ake adzamveka ngati bingu kuchokera ku malo ake opatulika. Zoonadi, adzakhuluma, kukalipira anthu ake, adzafuula kwambiri ngati anthu oponda mphesa, polimbana ndi anthu onse a pa dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake muwanenere iwo mau onse awa, ndi kuti kwa iwo, Yehova adzabangula kumwamba, nadzatchula mau ake mokhalamo mwake moyera; adzabangulitsira khola lake; adzafuula, monga iwo akuponda mphesa, adzafuulira onse okhala m'dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsopano iwe nenera mawu owatsutsa ndipo uwawuze kuti, “ ‘Yehova adzabangula kumwamba; mawu ake adzamveka ngati bingu kuchokera ku malo ake opatulika. Adzabangula mwamphamvu kukalipira dziko lake. Iye adzafuwula ngati anthu oponda mphesa, kukalipira onse amene akukhala pa dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace muwanenere iwo mau onse awa, ndi kuti kwa iwo, Yehova adzabangula kumwamba, nadzachula mau ace mokhalamo mwace moyera; adzabangulitsira khola lace; adzapfuula, monga iwo akuponda mphesa, adzapfuulira onse okhala m'dziko lapansi.