Jeremiah 25:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Phokoso lalikululo lidzamveka pa dziko lonse lapansi, chifukwa Chauta akuŵazenga mlandu anthu a mitundu yonse. Akuti aweruza anthu onse, ndipo oipa adzaphedwa ndi lupanga, akuterotu Chauta.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Phokoso lidzadza ku malekezero a dziko lapansi; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi mitundu ya anthu, adzatsutsana ndi anthu onse; koma oipa, adzawapereka kulupanga, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Phokoso lalikulu lidzamveka mpaka kumalekezero a dziko lonse lapansi, chifukwa Yehova adzazenga mlandu anthu a mitundu yonse; adzaweruza mtundu wonse wa anthu ndipo oyipa adzawapha ndi lupanga,’ ” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Phokoso lidzadza ku malekezero a dziko lapansi; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi mitundu ya anthu, adzatsutsana ndi anthu onse; koma oipa, adzawapereka kulupanga, ati Yehova.