Jeremiah 25:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Onani, tsoka likuti likachoka pa mtundu wina likukagwa pa mtundu winanso. Ndipo ku malekezero a dziko lapansi kukuyambika mphepo yamkuntho.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wa makamu atero, Taonani, zoipa zidzatuluka kumtundu kunka m'mitundu, ndipo namondwe adzauka kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Taonani! Mavuto akuti akachoka pa mtundu wina akukagwa pa mtundu wina; mphepo ya mkuntho ikuyambira ku malekezero a dziko.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wa makamu atero, Taonani, zoipa zidzaturuka ku mtundu kunka m'mitundu, ndipo namondwe adzauka kucokera ku malekezero a dziko lapansi.