Jeremiah 25:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku limenelo, onse ophedwa ndi Chauta adzangoti vuu pa dziko lonse lapansi. Palibe amene adzaŵalire, kapena kukaŵaika m'manda. Adzangosiyidwa ngati ndoŵe ponseponse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kuchokera ku malekezero ena a dziko lapansi kunka ku malekezero ena a dziko lapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku limenelo, onse ophedwa ndi Yehova adzangoti mbwee ponseponse, pa dziko lonse lapansi. Palibe amene adzawalire kapena kusonkhanitsa mitemboyo kuti ikayikidwe mʼmanda, koma idzakhala mbwee ngati ndowe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kucokera ku malekezero ena a dziko lapansi kunka ku malekezero ena a dzikolapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka.