Jeremiah 25:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu abusa lirani kwambiri, fuulani kwamphamvu. Inu atsogoleri a anthu anga, dzolani phulusa. Nthaŵi yanu yokaphedwa yafika, ndipo mudzachita kuphedwa ngati nkhosa zamphongo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuwani, inu abusa, lirani, gubudukani, inu akulu a zoweta; pakuti masiku a kuphedwa kwanu akwanira ndithu, ndipo ndidzakuphwanyani inu, ndipo mudzagwa ngati chotengera chofunika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Khetsani misozi ndi kufuwula mwamphamvu, abusa inu; gubudukani pa fumbi, inu atsogoleri a nkhosa. Pakuti nthawi yanu yophedwa yafika; mudzagwa ndi kuphwanyika ngati mbiya yabwino kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuwani, inu abusa, lirani, gubudukani, inu akuru a zoweta; pakuti masiku a kuphedwa kwanu akwanira ndithu, ndipo ndidzakuphwanyani inu, ndipo mudzagwa ngati cotengera cofunika.