Jeremiah 25:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndidzaitana mafuko onse akumpoto, pamodzi ndi mtumiki wanga Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni. Ndidzaŵatuma kuti adzathire nkhondo dzikoli ndi anthu ake, ndiponso anthu a mitundu ina yozungulira dzikoli. Ndidzaŵaononga kwathunthu ndi kuŵasandutsa chinthu chonyansa, chonyozeka ndiponso chochititsa manyazi mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo pa dziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndidzayitana mafuko onse akumpoto, pamodzi ndi mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni,” akutero Yehova, “ndipo adzathira nkhondo dziko lino ndi anthu ake pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu ozungulira dzikoli. Ndidzawawononga kwathunthu ndi kuwasandutsa chinthu chochititsa mantha ndi chonyozeka, mpaka muyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
taonani, Ine ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo pa dziko lino, ndi pa okhalamo ace onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo cizizwitso, ndi cotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.