Jeremiah 26:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuluakulu a ku Yuda atamva zimene zinkachitikazo, adanyamuka kuchokera ku nyumba ya mfumu kupita ku Nyumba ya Chauta, nakakhala pa bwalo lao ku chipata chatsopano cha Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene akulu a Yuda anamva zimenezi, anakwera kutuluka kunyumba ya mfumu kunka kunyumba ya Yehova; ndipo anakhala pa khomo la chipata chatsopano cha nyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma nduna za ku Yuda zitamva zomwe zinachitikazi, zinanyamuka kuchokera ku nyumba yaufumu kupita ku Nyumba ya Yehova, nakakhala pamalo pawo, pa Chipata Chatsopano cha Nyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene akuru a Yuda anamva zimenezi, anakwera kuturuka ku nyumba ya mfumu kunka ku nyumba ya Yehova; ndipo anakhala pa khomo la cipata catsopano ca nyumba ya Yehova.