Jeremiah 26:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo ansembe ndi aneneri adauza akuluakuluwo ndi anthu ena onse kuti, “Munthu ameneyu ndi woyenera kumupha, chifukwa choti amalosa zoipa za mzinda uno, monga inu nomwe mwadzimvera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ansembe ndi aneneri ananena kwa akulu ndi kwa anthu onse, kuti, Munthu uyu ayenera kufa; pakuti wanenera mudzi uwu monga mwamva ndi makutu anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo ansembe ndi aneneri anawuza ndunazo pamodzi ndi anthu onse kuti, “Munthu uyu ayenera kuphedwa chifukwa amalosera zoyipira mzinda uno. Inu mwadzimvera nokha zimenezi!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ansembe ndi aneneri ananena kwa akuru ndi kwa anthu onse, kuti, Munthu uyu ayenera kufa; pakuti wanenera mudzi uwu monga mwamva ndi makutu anu.