Jeremiah 26:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati tsopano mukonza makhalidwe anu ndi ntchito zanu zomwe, ndi kuyamba kumvera mau a Chauta Mulungu wanu, ndiye kuti Iye adzakhululuka osakulangani monga m'mene adaaganizira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tsopano konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndi kumvera mau a Yehova Mulungu wanu; ndipo Yehova adzaleka choipa chimene ananenera inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano konzani njira zanu ndi zochita zanu ndipo mverani Yehova Mulungu wanu. Mukatero ndiye kuti Yehova adzaleka osakupatsani chilango chimene ankati akupatseni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tsopano konzani njira zanu ndi macitidwe anu, ndi kumvera mau a Yehova Mulungu wanu; ndipo Yehova adzaleka coipa cimene ananenera inu.