Jeremiah 26:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ineyo ndili m'manja mwanu. Mundichite chilichonse chimene chikukomereni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ine, taonani, ndili m'manja anu; mundichitire ine monga mokomera ndi moyenera m'maso anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kunena za ine, ndili mʼmanja mwanu; mundichite chilichonse chimene mukuganiza kuti ndi chabwino ndi choyenera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ine, taonani, ndiri m'manja anu; mundicitire ine monga mokomera ndi moyenera m'maso anu.