Jeremiah 26:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsono mudziŵe kuti mukangondipha, ndiye kuti inuyo pamodzi ndi mzinda uno ndi anthu onse okhalamo, mudzapalamula mlandu wokhetsa magazi a munthu wosalakwa. Ndithudi, nzoona kuti Chauta ndiye adandituma kwa inu, kuti mumve zonse ndikunenazi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mudziwe ndithu kuti, ngati mudzandipha ine, mudzadzitengera nokha mwazi wosachimwa, ndi pa mudzi uwu, ndi pa okhalamo ake; pakuti mwa ntheradi Yehova wandituma kwa inu kuti ndinene mau onse awa m'makutu anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komatu dziwani kuti ngati mundipha, inu pamodzi ndi mzinda uno ndi onse amene amakhala muno, mudzapalamula mlandu wokhetsa magazi a munthu wosalakwa. Ndithudi Yehova anandituma kuti ndidzayankhule mawu onsewa inu mukumva.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mudziwe ndithu kuti, ngati mudzandipha ine, mudzadzitengera nokha mwazi wosacimwa, ndi pa mudzi uwu, ndi pa okhalamo ace; pakuti mwa ntheradi Yehova wandituma kwa inu kuti ndinene mau onse awa m'makutu anu.