Jeremiah 26:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nthaŵi imene Hezekiya anali mfumu ya ku Yuda, Mika wa ku Moreseti ankalosa, ndipo adauza anthu onse a ku Yuda kuti Chauta Wamphamvuzonse akuti, “ ‘Ziyoni adzalimidwa ngati munda. Yerusalemu adzasanduka bwinja, phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mika Mmoreseti ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mʼmasiku a Hezekiya mfumu ya ku Yuda, Mika wa ku Moreseti ankalosera. Iye ankawuza anthu kuti Yehova Wamphamvuzonse akuti, “ ‘Ziyoni adzatipulidwa ngati munda, Yerusalemu adzasanduka bwinja, ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango yowirira.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mika Mmorasi ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.