Jeremiah 26:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga kodi mfumu Hezekiya ndi anthu onse a ku Yuda adamupha amene uja? Kodi suja mfumu idaopa Chauta nipempha kuti aikomere mtima? Ndipo suja Chauta adaleka osaŵapatsa chilango chimene adaati aŵalange nacho? Koma ife tili pafupi kudziitanira tsoka lalikulu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi Yuda wonse anamupha iye konse? Kodi sanamuope Yehova, napembedzera Yehova, ndipo Yehova analeka choipa chimene ananenera iwo? Chotero tidzaichitira miyoyo yathu choipa chachikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi Hezekiya mfumu ya ku Yuda ndi anthu onse anamupha amene uja? Kodi suja mfumu inaopa Yehova ndi kupempha kuti ayikomere mtima? Ndipo suja Yehova anasintha maganizo ake nʼkuleka kuwalanga monga mʼmene anakonzera? Ifetu tikudziyitanira tsoka lalikulu!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi Yuda wonse anamupha iye konse? kodi sanamuopa Yehova, napembedzera Yehova, ndipo Yehova analeka coipa cimene ananenera iwo? Cotero tidzaicitira miyoyo yathu coipa cacikuru.