Jeremiah 26:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kaime m'bwalo la Nyumba ya Chauta. Ndipo ukalankhule kwa anthu onse okhala m'mizinda ya ku Yuda, amene amakapembedza ku Nyumba imeneyo. Ukaŵauze zonse zimene ndakulamula kuti ukanene, osasiyapo kanthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova atero: Ima m'bwalo la nyumba ya Yehova, ndi kunena kwa midzi yonse ya Yuda, imene imadza kudzagwadira m'nyumba ya Yehova, mau onse amene ndikuuza iwe kuti unene kwa iwo; usasiyepo mau amodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kayime mʼbwalo la Nyumba ya Yehova. Ndipo ukayankhule kwa anthu onse okhala mʼmizinda ya ku Yuda amene amabwera kudzapembedza ku Nyumba ya Yehova. Ukawawuze zonse zomwe ndakulamula; usakasiyeko ndi mawu amodzi omwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova atero: Ima m'bwalo la nyumba ya Yehova, ndi kunena kwa midzi yonse ya Yuda, imene imadza kudzagwadira m'nyumba ya Yehova, mau onse amene ndikuuza iwe kuti unene kwa iwo; usasiyepo mau amodzi.