Jeremiah 26:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Padaalinso munthu wina amene ankalosa m'dzina la Chauta, dzina lake Uriya mwana wa Semaya wa ku Kiriyati-Yearimu. Iyeyo adaalosanso zodzagwera mzinda uno ndi dziko lino monga momwe adachitira Yeremiya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panalinso munthu amene ananenera m'dzina la Yehova, Uriya mwana wake wa Semaya wa ku Kiriyati-Yearimu; ndipo iye ananenera mudzi uwu ndi dziko lino monga mwa mau onse a Yeremiya;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
(Panalinso munthu wina, Uriya mwana wa Semaya wa ku Kiriati-Yeyarimu, amene ankalosera mʼdzina la Yehova. Iyeyu analosera za mzinda uno ndi dziko lino monga mmene wachitira Yeremiya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panalinso munthu amene ananenera m'dzina la Yehova, Uriya mwana wace wa Semaya wa ku Kiriati Yearimu; ndipo iye ananenera mudzi uwu ndi dziko lino monga mwa mau lonse a Yeremiya;