Jeremiah 26:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Yehoyakimu ndi akuluakulu ake onse ndiponso ankhondo ake, atamva zimene adaanena, adaafuna kumupha. Uriya atamva choncho, adachita mantha, nathaŵira ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo pamene Yehoyakimu mfumu, ndi amphamvu ake onse, ndi akulu onse, anamva mau ake, mfumu inafuna kumupha iye; koma pamene Uriya anamva, anaopa, nathawa, nanka ku Ejipito;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Yehoyakimu, ankhondo ake onse ndi nduna zake anamva mawu akewo, ndipo anafuna kumupha. Koma Uriya atamva zimenezi, anachita mantha nathawira ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo pamene Yehoyakimu mfumu, ndi amphamvu ace onse, ndi akuru onse, anamva mau ace, mfumu inafuna kumupha iye; koma pamene Uriya anamva, anaopa, nathawa, nanka ku Aigupto;