Jeremiah 26:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwowo adakagwira Uriya ku Ejipito komweko, nkubwera naye kwa mfumu Yehoyakimu. Mfumuyo idalamula kuti Uriyayo aphedwe, ndipo mtembo wake adakauika ku manda a anthu wamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo anamtulutsa Uriya m'Ejipito, nanka naye kwa Yehoyakimu mfumu; amene anamupha ndi lupanga, naponya mtembo wake m'manda a anthu achabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anakamutenga Uriya ku Igupto kuja nabwera naye kwa Mfumu Yehoyakimu. Iye anamupha ndi lupanga ndipo mtembo wake anakawutaya ku manda a anthu wamba).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo anamturutsa Uriya m'Aigupto, nanka naye kwa Yehoyakimu mfumu; amene anamupha ndi lupanga, naponya mtembo wace m'manda a anthu acabe.