Jeremiah 26:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwina mwake nkutheka kuti adzamvera, ndipo aliyense adzaleka machimo ake. Tsono ndidzaleka osaŵapatsa chilango chimene ndidaati ndiŵalange nacho, chifukwa cha ntchito zao zoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena adzamvera, nadzatembenuka, yense kusiya njira yake yoipa; kuti ndileke choipa, chimene ndinati ndiwachitire chifukwa cha kuipa kwa ntchito zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwina mwake adzamvera, ndipo aliyense adzatembenuka kuleka njira yake yoyipa. Ndiye ine ndidzaleka osapatsa chilango chimene ndinakonzekera kuti ndiwalange nacho chifukwa cha ntchito zawo zoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kapena adzamvera, nadzatembenuka, yense kusiya njira yace yoipa; kuti ndileke coipa, cimene ndinati ndiwacitire cifukwa ca kuipa kwa nchito zao.