Jeremiah 26:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yeremiya atatsiriza kulankhula zimene Chauta adamlamula kuti auze anthu onse, ansembe, aneneri ndi anthu onsewo adamgwira, namuuza kuti, “Ukuyenera kuphedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali, pamene Yeremiya anatha kunena mau onse amene Yehova anamuuza iye kuti anene kwa anthu onse, ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamgwira iye, ndi kuti, Udzafa ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yeremiya atangotsiriza kuwawuza anthu aja zonse zimene Yehova anamulamula kuti ayankhule, ansembe, aneneri pamodzi ndi anthu onse anamugwira ndipo anati, “Uyenera kuphedwa!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali, pamene Yeremiya anatha kunena mau onse amene Yehova anamuuza iye kuti anene kwa anthu onse, ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamgwira iye, ndi kuti, Udzafa ndithu.