Jeremiah 26:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chiyani walosa m'dzina la Chauta kuti Nyumba ino idzaonongedwa ngati Silo, ndipo kuti mzinda uno udzasanduka wopanda anthu, ngati chipululu?” Motero anthu onse adasonkhana nazinga Yeremiya m'Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Bwanji mwanenera m'dzina la Yehova, kuti, Nyumba iyi idzafanana ndi Silo, mudzi uwu udzakhala bwinja lopanda wokhalamo? Ndipo anthu onse anamsonkhanira Yeremiya m'nyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chiyani walosera mʼdzina la Yehova kuti Nyumba ino idzakhala ngati Silo ndipo mzinda uno udzakhala wopanda anthu ngati chipululu?” Anthu onse anamuzungulira Yeremiya mʼNyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Bwanji mwanenera m'dzina la Yehova, kuti, Nyumba iyi idzafanana ndi Silo, mudzi uwu udzakhala bwinja lopanda wokhalamo? Ndipo anthu onse anamsonkhanira Yeremiya m'nyumba ya Yehova.