Jeremiah 27:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mtundu wina uliwonse umene udzagonjera mfumu ya ku Babiloni ndi kumaitumikira, ndidzausiya kuti ukhale m'dziko lake, kuti uzilima ndi kumakhala kumeneko,” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mtundu umene udzaika khosi lao pansi pa goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye, mtundu umene ndidzaulola ukhalebe m'dziko lao, ati Yehova; ndipo adzalilima, nadzakhala momwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati mtundu wina uliwonse udzagonjera mfumu ya ku Babuloni ndi kuyitumukira, ndidzawusiya kuti ukhale mʼdziko lake kuti uzilima ndi kukhalamo, akutero Yehova.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mtundu umene udzaika khosi lao pansi pa gori la mfumu ya ku Babulo, ndi kumtumikira iye, mtundu umene ndidzaulola ukhalebe m'dziko lao, ati Yehova; ndipo adzalilima, nadzakhala momwemo.