Jeremiah 27:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mau okhaokhawo ndidauzanso Zedekiya mfumu ya ku Yuda, ndidati: Mugonjere ulamuliro wa mfumu ya ku Babiloni ndi kumaitumikira iyoyo pamodzi ndi anthu ake. Mukatero mudzapulumutsa moyo wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinanena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda monga mau onse amenewa, kuti, Longani makosi anu m'goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye ndi anthu ake, ndipo mudzakhala ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uthenga womwewu ndinawuzanso Hezekiya mfumu ya Yuda. Ndinati, “Gonjerani mfumu ya ku Babuloni. Itumikireni iyoyo pamodzi ndi anthu ake ndipo mudzakhala ndi moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinanena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda monga mau onse amenewa, kuti, Longani makosi anu m'gori la mfumu ya ku Babulo, ndi kumtumikira iye ndi anthu ace, ndipo mudzakhala ndi moyo.