Jeremiah 27:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musaŵamvere aneneri okuuzani kuti musadzatumikire mfumu ya ku Babiloni. Akukuloserani zabodza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamvere mau a aneneri amene anena ndi inu, kuti, simudzamtumikira mfumu ya ku Babiloni; pakuti akunenerani zonama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musamvere mawu a aneneri akamakuwuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya ku Babuloni,’ chifukwa zimene akukuloseranizo nʼzabodza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamvere mau a aneneri amene anena ndi inu, kuti, simudzamtumikira mfumu ya ku Babulo; pakuti akunenerani zonama.