Jeremiah 27:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sindidaŵatume ndine, ngakhale iwowo akuti amalosa m'dzina langa. Motero ndidzakupirikitsani, ndipo mudzaonongeka inuyo pamodzi ndi aneneri amene amakuloseraniwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sindinawauma iwo, ati Yehova, koma anenera zonama m'dzina langa; kuti ndikupirikitseni inu, kuti mudzathedwe, inu, ndi aneneri amene anenera kwa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sindinawatume ngakhale iwo akulosera mʼdzina langa. Nʼchifukwa chake, ndidzakupirikitsani ndipo mudzawonongeka kotheratu, inu pamodzi ndi aneneri amene akunenera zabodza kwa inu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti sindinawatuma iwo, ati Yehova, koma anenera zonama m'dzina langa; kuti ndikupitikitseni inu, kuti mudzathedwe, inu, ndi aneneri amene anenera kwa inu.