Jeremiah 27:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pambuyo pake ndidauza ansembe pamodzi ndi anthu ena onse kuti Chauta akunena kuti: Musaŵamvere aneneri anu amene amakuuzani kuti, ‘Ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta adzazibwezanso mwamsanga kuchokera ku Babiloni.’ Iwowo akungokuloserani zabodza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso ndinanena kwa ansembe ndi kwa anthu onsewa, kuti, Yehova atero: Musamvere mau a aneneri anu amene akunenerani inu, kuti, Taonani, zipangizo za nyumba ya Yehova zidzatengedwanso ku Babiloni posachedwa; pakuti akunenerani inu zonama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ndinawuza ansembe pamodzi ndi anthu ena onse kuti, “Yehova akuti: Musamvere aneneri amene akumanena kuti, ‘Posachedwapa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zibwera kuchokera ku Babuloni.’ Iwowo akunenera zabodza kwa inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso ndinanena kwa ansembe ndi kwa anthu onsewa, kuti, Yehova atero: Musamvere mau a aneneri anu amene akunenerani inu, kuti, Taonani, zipangizo za nyumba ya Yehova zidzatengedwanso ku Babulo posacedwa; pakuti akunenerani inu zonama.