Jeremiah 27:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati iwo ndi aneneridi ndipo ngati ali ndi mau a Chauta, apemphere kwa Chauta Wamphamvuzonse kuti ziŵiya zimene zidatsala m'Nyumba ya Chauta ndiponso m'nyumba ya mfumu ku Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati ndiwo aneneri, ndipo ngati mau a Yehova ali ndi iwo, tsopano apembedzere Yehova wa makamu, kuti zipangizo zotsala m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu, zisanke ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati iwo ndi aneneri ndipo ali ndi mawu a Yehova, apempheretu kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti ziwiya zimene zatsala mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndiponso mu Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati ndiwo aneneri, ndipo ngati mau a Yehova ali ndi iwo, tsopano apembedzere Yehova wa makamu, kuti zipangizo zotsala m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu, zisanke ku Babulo.