Jeremiah 27:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimenezi Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni sadazitenge pa nthaŵi imene ankatenga ukapolo Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, kuchoka naye ku Yerusalemu kupita naye ku Babiloni pamodzi ndi atsogoleri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
zimene sanazitenge Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, pamene anamtenga ndende Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Babiloni; ndi akulu onse a Yuda ndi Yerusalemu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Izi ndi zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni sanatenge pamene anatenga ukapolo Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda kupita ku Babuloni kuchokera ku Yerusalemu, pamodzi ndi anthu olemekezeka a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
zimene sanazitenga Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo, pamene anamtenga ndende Yekoniya mwana wace wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, kucokera ku Yerusalemu kunka ku Babulo; ndi akuru onse a Yuda ndi Yerusalemu;