Jeremiah 27:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidalenga dziko lapansi ndi mphamvu zanga ndi nyonga zanga. Ndidalenga anthu ndi nyama pa dziko lapansi, ndipo ndimalipereka kwa amene ndimamuwona kuti ndi woyenera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ine ndinalenga dziko lapansi, anthu ndi nyama zokhala m'dzikomo, ndi mphamvu yanga yaikulu ndi mkono wanga wotambasuka; ndipo ndinapereka ilo kwa iye amene ayenera pamaso panga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi mphamvu zanga ndi dzanja langa lamphamvu ndinalenga dziko lapansi ndi anthu ake onse pamodzi ndi nyama zili mʼmenemo, ndipo ndimalipereka kwa aliyense amene ndikufuna.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ine ndinalenga dziko lapansi, anthu ndi nyama zokhala m'dzikomo, ndi mphamvu yanga yaikuru ndi mkono wanga wotambasuka; ndipo ndinapereka ilo kwa iye amene ayenera pamaso panga.