Jeremiah 27:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano ndapereka maiko onseŵa kwa Nebukadinezara mtumiki wanga, mfumu ya ku Babiloni. Ndampatsanso nyama zonse zakuthengo kuti zizimtumikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsopano ndapereka maiko onse awa m'manja a Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga; ndiponso nyama za kuthengo ndampatsa iye kuti zimtumikire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano ndidzapereka mayiko anu onse kwa mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni. Ndamupatsanso nyama zakuthengo zonse kuti zimutumikire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsopano ndapereka maiko onse awa m'manja a Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo, mtumiki wanga; ndiponso nyama za kuthengo ndampatsa iye kuti zimtumikire.