Jeremiah 27:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a mitundu yonse adzamtumikira iyeyo, mwana wake ndi mdzukulu wake, mpaka itakwana nthaŵi yoti dziko lake liwonongedwe. Pamenepo anthu a mitundu yambiri ndi mafumu amphamvu adzagonjetsa ufumu wakewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo amitundu onse adzamtumikira iye, ndi mwana wake, ndi mdzukulu wake, mpaka yafika nthawi ya dziko lake; ndipo amitundu ambiri ndi mafumu akulu adzamuyesa iye mtumiki wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a mitundu yonse adzamutumikira iyeyo, mwana wake ndi chidzukulu chake mpaka nthawi itakwana yoti dziko lake liwonongedwe. Pamenepo mitundu yambiri ndi mafumu amphamvu adzamugonjetsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo amitundu, onse adzamtumikira iye, ndi mwana wace, ndi mdzukulu wace, mpaka yafika nthawi ya dziko lace; ndipo amitundu ambiri ndi mafumu akuru adzamuyesa iye mtumiki wao.