Jeremiah 27:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma ngati anthu a mtundu wina uliwonse kapena a dziko lina lililonse adzakana kutumikira Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, kapena kugonjera ulamuliro wake, Ineyo ndidzaŵalanga ndi nkhondo, njala ndi mliri, mpaka nditaŵapereka m'manja mwake kotheratu,” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babiloni, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola, mpaka nditatha onse ndi dzanja lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Koma ngati anthu a mtundu wina uliwonse kapena ufumu wina uliwonse adzakana kutumikira Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kapena kusenza goli lake, Ine ndidzalanga mtundu umenewo ndi lupanga, ndi njala ndi mliri, akutero Yehova, mpaka nditawapereka mʼmanja mwake kotheratu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babulo, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi caola, mpaka nditatha onse ndi dzanja lace.