Jeremiah 28:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka chomwecho mwezi wachisanu wa chaka chachinai, Zedekiya ataloŵa ufumu wa ku Yuda, Hananiya mwana wa Azuri mneneri wa ku Gibiyoni, adalankhula nane ku Nyumba ya Chauta. Ansembe ndi anthu onse alikumva, iye adati,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali chaka chomwecho, poyamba Zedekiya kukhala mfumu ya Yuda, chaka chachinai, mwezi wachisanu, kuti Hananiya mwana wa Azuri mneneri, amene anali wa ku Gibiyoni, ananena ndi ine m'nyumba ya Yehova, pamaso pa ansembe ndi pa anthu onse, kuti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chaka chomwecho mwezi wachisanu wa chaka chachinayi, poyambirira pa ulamuliro wa Zedekiya mfumu ya Yuda, mneneri Hananiya mwana wa Azuri, amene amachokera ku Gibiyoni, anandiwuza ine mʼNyumba ya Yehova pamaso pa ansembe ndi anthu onse kuti,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali caka comweco, poyamba Zedekiya kukhala mfumu ya Yuda, caka cacinai, mwezi wacisanu, kuti Hananiya mwana wa Azuri mneneri, amene anali wa ku Gibeoni, ananena ndi ine m'nyumba ya Yehova, pamaso pa ansembe ndi pa anthu onse, kuti,