Jeremiah 28:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adauza anthu onse kuti, “Chauta akuti, ‘Umu ndimo m'mene ndidzathyolera goli laukapolo la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni. Ndidzalichotsa m'khosi mwa anthu a mitundu yonse zisanathe zaka ziŵiri.’ ” Zitatero mneneri Yeremiya adachokapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hananiya ananena pamaso pa anthu onse, kuti, Yehova atero: Chomwecho ndidzathyola goli la Nebukadinezara mfumu ya Babiloni zisanapite zaka ziwiri zamphumphu kulichotsa pa khosi la amitundu onse. Ndipo Yeremiya mneneri anachoka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo anawuza anthu onse kuti, “Yehova akuti, ‘Umu ndi mmene ndidzathyolere goli la Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni mʼkhosi mwa anthu a mitundu yonse pasanathe zaka ziwiri.’ ” Zitatero, mneneri Yeremiya anachoka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hananiya ananena pamaso pa anthu onse, kuti, Yehova atero: Comweco ndidzatyola gori la Nebukadinezara mfumu ya Babulo zisanapite zaka ziwiri zamphumphu kulicotsa pa khosi la amitundu onse. Ndipo Yeremiya mneneri anacoka.