Jeremiah 28:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Ndaika goli lachitsulo m'khosi mwa anthu a mitundu yonseyi, kuti azitumikira Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni. Adzamutumikiradi, ndipo ndampatsanso ulamuliro ngakhale pa nyama zakuthengo.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Ndaika goli lachitsulo pa khosi la amitundu onsewa, kuti amtumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo adzamtumikira iye; ndipo ndampatsanso nyama za kuthengo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Ndidzayika goli lachitsulo mʼkhosi mwa anthu a mitundu yonseyi kuti atumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo iwo adzamutumikiradi. Ndipo ndamupatsanso ulamuliro ngakhale pa nyama zakuthengo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Ndaika gori lacitsulo pa khosi la amitundu onsewa, kuti amtumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo; ndipo adzamtumikira iye; ndipo ndampatsanso nyama za kuthengo.