Jeremiah 28:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yeremiya adauza Hananiya kuti, “Mvera, iwe Hananiya, Chautatu sadakutume, ndipo iweyo wanyenga anthuŵa kuti azimvera ulosi wabodza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yeremiya mneneri ananena kwa Hananiya mneneri, Tamvatu, Hananiya; Yehova sanakutume iwe; koma ukhulupiritsa anthu awa zonama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mneneri Yeremiya anawuza mneneri Hananiya kuti, “Tamvera, Hananiya! Iweyo Yehova sanakutume, koma iwe wanyenga anthuwa kuti akhulupirire zabodza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yeremiya mneneri ananena kwa Hananiya mneneri, Tamvatu, Hananiya; Yehova sanakutuma iwe; koma ukhulupiritsa anthu awa zonama.