Jeremiah 28:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, ‘Chenjera, ndidzakuchotsa pa dziko lapansi. Ufa chaka chino chisanathe, chifukwa chakuti wakhala ukulalikira zopandukira Chauta.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Yehova atero, Taona, Ine ndidzakuchotsa iwe kudziko; chaka chino udzafa, pakuti wanena zopikisana ndi Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Yehova akuti, ‘Ndatsala pangʼono kukuchotsa pa dziko lapansi. Iwe ufa chaka chino chisanathe, chifukwa wakhala ukulalikira zowukira Yehova.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Yehova atero, Taona, Ine ndidzakucotsa iwe kudziko; caka cino udzafa, pakuti wanena zopikisana ndi Yehova.