Jeremiah 28:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zisanathe zaka ziŵiri, ndidzabwezera ziŵiya zonse za ku Nyumba yanga ku malo ano, zimene Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adazichotsa kuno kupita nazo ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zisanapite zaka ziwiri zamphumphu Ine ndidzabwezeranso kumalo kuno zipangizo zonse za m'nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anazichotsa muno, kunka nazo ku Babiloni;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pasanathe zaka ziwiri ndidzabweretsa pa malo ano ziwiya zonse za ku Nyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anazichotsa pa malo pano ndi kupita nazo ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zisanapite zaka ziwiri zamphumphu Ine ndidzabwezeranso kumalo kuno zipangizo zonse za m'nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anazicotsa muno, kunka nazo ku Babulo;