Jeremiah 28:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzambwezanso ku malo ano Yehoyakini, mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda. Ndidzabweza akapolo onse ochokera ku Yuda amene adatengedwa kupita ku Babiloni. Motero ndidzathyola goli laukapolo la mfumu ya ku Babiloni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndidzabweranso kumalo kuno Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi am'nsinga onse a Yuda, amene ananka ku Babiloni, ati Yehova: pakuti ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzabweretsanso pa malo pano Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda pamodzi ndi akapolo ena onse ochokera ku Yuda amene anapita ku Babuloni,’ akutero Yehova, ‘chifukwa ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babuloni.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndidzabwezeranso kumalo kuno Yekoniya mwana wace wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi am'nsinga onse a Yuda, amene ananka ku Babulo, ati Yehova: pakuti ndidzatyola gori la mfumu ya ku Babulo.