Jeremiah 28:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ngati mneneri alosa za mtendere, zimene walosazo zikachitikadi, pamenepo zidzadziŵika kuti Chauta adamtumadi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mneneri amene anenera za mtendere, pamene mau a mneneri adzachitidwa, pamenepo mneneri adzadziwika, kuti Yehova anamtuma ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mneneri amene amalosera zamtendere adzadziwika kuti ndi woona ndi kuti watumidwa ndi Yehova ngati zimene wanenera zachitikadi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mneneri amene anenera za mtendere, pamene mau a mneneri adzacitidwa, pamenepo mneneri adzadziwika, kuti Yehova anamtuma ndithu.